"OYIMBIRA SANAGWIRE BWINO NTCHITO" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati oyimbira pa masewero awo ndi Silver Strikers analephera kuteteza osewera awo pa masewerowa ndipo zimenezi sizinamukondweretse.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-2 ndi timu ya Silver pa bwalo la Silver ndipo wati masewero anali abwino chovuta ndi choti agonja.
"Anali masewero abwino, tasewera bwino koma taluza anzathu awina tiwayamikire. Oyimbira sanali bwino, ana ambiri amapondedwa, wina wapondedwa khosi koma palibepo angakhale kadi yomwe oyimbira anapereka." Anatero Kaunda.
Timuyi tsopano ili pa nambala yachikhumi (10) ndi mapointsi asanu ndi atatu (8) pa masewero asanu ndi atatu (8) omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores