"ANZATHUWA ATHANDIZIDWA NDI OYIMBIRA" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu ya MAFCO yapindula kwambiri ndi oyimbira mmasewero omwe matimuwa amakumana ati ponena kuti amakanika kugwira ntchito moyenerera.
Chirwa amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 ndi timu ya MAFCO ndipo wati osewera a MAFCO amangogwa atagoletsa koma oyimbira sanapangepo kanthu.
"Ndikukhulupilira kuti anzathuwa Ali ndi malamulo awo omwe amayendetsera nde koma anzathuwa atagoletsa anayamba kumangochedwetsa nthawi Pena kumangogwa asanavulale nde apindula kwambiri anzathuwa chifukwa oyimbira wakanika kuyendetsa masewerowa." Anatero Chirwa.
Iye watinso timu yake ikukumana ndi mavuto ogoletsa koma tsopano yapezako osewera angapo paulendo wawo ku chigawo chapakati omwe awathandizire zikatheka.
FOMO ili pa nambala 13 pomwe ili ndi mapointsi 7 pa masewero 8 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores