"TIMAFUNIKA KUPAMBANA" - MZUNGA
Wachiwiri kwa timu ya MAFCO, Jimmy Mzunga, wati timu yake imafunitsitsa kupeza chipambano pomwe inakumana ndi FOMO ndipo akondwa poti achipezadi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-0 ndi chigoli cha Marshall Maluwa zomwe zawathandiza kusuntha kwambiri pa ndandanda wa matimu ndipo wati akondwa.
"Timafunitsitsa kupambanaku nde ndife wokondwa kwambiri. Chipambano chabwera mu nthawi yake chifukwa tsopano tikusuntha kusiyana ndi mmene tinayambira muja." Iye anatero.
Pa masewero atatu apitawa, timuyi yakwanitsa kupeza mapointsi asanu ndi awiri (7) zomwe zatithandiza kwambiri timuyi.
Iyo yafika pa nambala 11 mu ligi pomwe ali ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pamasewero asanu ndi atatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores