"SINDINAKHUTIRE NDI POINT IMODZI" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati siwokhutira ndi kupeza point imodzi ku chigawo chakumpoto pomwe wati amafunitsitsa kupeza onse atatu.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 1-1 ndi Baka City ndipo wayamikira anyamata ake potsatira malangizo ndi cholinga choti apeze chigoli chobwenzera mmasewerowa.
"Anali masewero ovuta chifukwa Baka inabwera nde Inatidzidzimutsa ndi chigoli mchigawo choyamba koma mchigawo chachiwiri ndinawauza anyamata kuti timenye mpira wathu chifukwa poyamba timavutika ndi mphepo komanso anzathuwa amangochimenya nde zinatheka mpaka tinapeza chigoli." Anatero Nginde.
Timu ya Creck Sporting tsopano ili pa nambala 12 pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi atatu (8) pa masewero asanu ndi atatu (8) mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores