"MASAPOTA AMAFUNA KUPAMBANA KOMA ADEKHE" - KADZUWA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macnerbert Kadzuwa, wati masapota omwe amakuwa potsutsana ndi ziganizo zake adekhe poti pali masewero ochuluka omwe asewere kutsogoloku.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 ndi Civo United pa bwalo la Karonga lachisanu ndipo wati masapota amafuna kuwina mpake akukuwa koma afatse poti mtunda ukadalipo.
"Masapota ndi khalidwe lawo loti amafuna nthawi zonse kupambana koma adekhe chifukwa tatsala ndi masewero ochuluka omwe atithandize kuti tibwerere pomwe tinali chaka chatha nde atipangebe sapoti kuti tichite bwino." Anatero Kadzuwa.
Iye watinso bungwe la Super League of Malawi nthawi zina lizitha kuwamva zodandaula zawo poti maulendo awo amakhala ataliatali nde amatopa.
Timuyi yapambana kamodzi , kufanana mphamvu kawiri ndikugonja kasanu pomwe ali ndi mapointsi asanu pa masewero 8 pa nambala 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores