"MKWIYO WA CIVO TIKAPHWESERA PA SILIVER" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yake yakonzeka kuthetsa mbiri ya timu ya Silver Strikers kuti sinagonje mu ligi pomwe akuyang'ana zoyigonjetsa akakumana.
Iye wayankhula patsogolo pa masewero omwe aliko loweruka pa bwalo la Silver ku Lilongwe ndipo wati mantha palibe poti ali ndi mkwiyo kamba kofanana mphamvu ndi Civo ndipo akaphwetsera pa mabanker.
"Takonzekera bwino kwambiri mukudziwa kuti tikuchoka kofanana mphamvu ndi Civo nde tili ndi mkwiyo omwe tikaphwetsere pa iwo. Akuchita bwino sanagonjeko koma chilichonse chili ndi chiyambi nde titha kukakhala oyamba kuwagonjetsa." Anatero Kaunda.
Iwe wati timu yake ilibe osewera aliyense ovulala ndipo chomwe akungodikira ndi kugonjetsa timuyi basi.
Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi anayi (9) pa masewero asanu ndi awiri (7).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores