"TIKUMUGWIRITSA NTCHITO BWINO" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wayamikira wosewera omwetsa zigoli kutimuyi, Emmanuel Savieli, kuti ndi mnyamata wodziwa ndipo akuthandiza timuyi.
Iwe wayankhula kutsatira kumwetsa zigoli ziwiri zomwe zathandiza timuyi kugonjetsa Chitipa United 3-1 lachisanu ndipo wati iwo akudziwa momugwiritsa ntchito mwake.
"Akutithandiza ndipo akudziwa pofunikira kuima komanso wadziwana ndi anzake nde tikumugwira ntchito bwino." Anatero Makawa.
Katswiriyu ali pangongole kuchokera ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets ndipo ali ndi zigoli zisanu ndi chimodzi (6) pa masewero asanu ndi atatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores