"KU KARONGA TSOPANO TAKUZOLOWERA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati timu yake izikhala ngati ili pakhomo pomwe ikumane ndi Chitipa United lachisanu ati kamba koti azolowerako ku Karonga.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Karonga ndipo wati mavuto onse akonza kuti apeze chipambano.
"Pano tsopano tazolowera ku Karonga ndipo nyengo yake tayizolowera ndipo tizisewera ngati tili pakhomo. Akhale masewero ovuta kwambiri komabe ifeyo sitikufuna kupanga ngati zomwe tinapanga ndi Karonga nde tikufuna kupambana." Anatero Makawa.
Timu ya Civo ili pa nambala 11 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi atatu (8) pa masewero asanu ndi awiri yomwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores