"MASEWEROWA ALI PA LAMULO LA SULOM" - BANDA
Mlembi wamkulu wa bungwe la Super League of Malawi, Williams Banda, wati chomwe bungwe lawo likudziwa ndi choti Chitipa United ikumana ndi Civo United lachisanu.
Iye wati timu ya Chitipa ikuyenera kungopanga za malamulo ampira poti masewerowa akutsata malamulo komanso kuti timu ya Civo inafika ku Karonga sabata yatha.
"Chitipa ikuyenera kupanga zampira chifukwa timu ya Civo inafika ku Karonga lachisanu sabata yatha nde iwowa ngati eni khomo akungoyenera kudzasewera masewerowa koma ngati satero Ife tipereka chilango chokhwima." Anatero Banda.
Timu ya Chitipa ikukana kusewera ndi Civo kamba koti masewerowa atsogozana ndi kuchokera koyenda Kwa Iwo ndipo sanakonzekere mokwana komanso kuti SULOM silinamve pempho lawo.
Padakali panopa, timuyi yanenetsa kuti sikasewera masewerowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores