"TIKUNGOKHALABE KUTI AMBUYE ATITSOGOLERE" - JIKA
Mwini wake watimu ya Bangwe All Stars, Mphatso Jika, wati zinthu sizikuyenda kutimu yake ndipo akungokhala kuti chilichonse chitachitike ndi chomwecho pomwe akukanika kuchika bwino mu chaka chino.
Iye amayankhula kutsatira kukanika kupeza chipambano kwa timuyi chaka chino angakhale kuti anakonzekera bwino komanso kukhala ndi zonse zoyenera.
"Zinthu sizikuyenda ndipo panopa tikungokhala ongolimba mtima kuti kaya tituluka mu ligi kaya tipanga bwanji chifukwa kukonzekera nde kunali kwabwino ndipo oseweranso abwino koma pa bwalo nde zikuvuta nde padakali panopa sizilibwino." Anatero Jika.
Timuyi inatenga osewera apamwamba ku matimu a Karonga United, Civo, Extreme FC ndi matimu ena pomwe ligiyi imayamba ndipo anakaseweranso ndi UD Songo yaku Mozambique pokonzekera ligiyi.
Iwo asewera masewero asanu ndi awiri (7) ndipo agonja kanayi (4) ndi kufanana mphamvu katatu (3) ndipo ali pa nambala 15.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores