WANDERERS YAKAGWADA KU FIFA
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yakagogoda ku bungwe loyendetsa mpira padziko lapansi la FIFA kuti liwathandize kuti mapepala a osewera waku Cameroon, Sama Thierry Tanjong, atheke ndikuti ayambe kutumikira timuyi.
Timuyi yachita chotere kamba koti padutsa masabata oyandikira atatu katswiriyu asakusewera chisayinireni mgwirizano wake kutimuyi kamba koti Football Association of Malawi siyinaperekebe kalata zovomereza katswiriyu kusewera.
Ndipo mkulu oyang'ana za nkhaniyi ku bungwe la FAM, Cassper Jangale, wati bungwe la mdziko la Cameron ndi lomwe silinatumize zikalata zokhudza katswiriyu.
"Zovuta zinanso ndi chifukwa choti osewerayu wakhala asakusewera mpira kuchokera mu October chaka cha 2022 nde ifeyo tinawalembera anzathuwo koma ngakhale anaonetsa chidwi, Iwo sanatiyankhebe." Anatero Jangale.
Padutsa masiku makumi awiri (20) katswiriyu atasaina mgwirizano wake komabe sangasewere analandire chilolezo zomwe zapangitsa Wanderers kukagwada ku FIFA pofuna
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores