CAF YAKHULUPILIRA AMALAWI ATATU
Bungwe loyendetsa mpira mu Africa la Confederation of African Football (CAF) lapereka maudindo kwa a Malawi atatu pa mpikisano wa masukulu amu Africa omwe uyambe pa 21 May ku Zanzibar.
Atatuwa ndi mkulu woona za mipikisano ku bungwe la Football Association of Malawi, Gomegzani Zakazaka komanso oyimbira awiri, Faith Gondwe komanso Wyson Mustafa, ndipo akagwira ntchito ku mpikisanowu.
Iwo adalinso pa mpikisano wa COSAFA wopitira ku mpikisano wa Africa yonse ndipo akuyembekezeka kunyamuka lero kulowera ku Zanzibar komwe mpikisanowu ukathe pa 24 May 2024.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores