"ANALI MASEWERO OVUTA KWAMBIRI" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati timu yake inayilora Civo kuti ipatsirane kwambiri mchifukwa chake sinakwanitse kuyigwira mpaka agonja.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Civo ndipo wati kutsegula komwe anachita mchigawo chachiwiri kunangowaputira nkhondo pomwe anapezetsa chigoli chachiwiri.
"Anali masewero ovuta kwambiri kutengera kuti tonse sitimachokera ku zotsatira zabwino koma tinawalora anzathu kukhala ndi mpira zomwe zinawapatsa mpata kuti apeze chigoli. Mchigawo chachiwiri tinasintha kuti tipanikize koma anagoletsa zomwe zinawafoola anyamata." Anatero Bunya.
Timuyi ikumane ndi Silver Strikers mmasewero awo otsatira ndipo ili ndi point imodzi pa nambala 13 pa masewero awiri mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores