"NDAKHUTIRA NDI ZOTSATIRAZI" - GONDWE
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe, wati wakhutira ndi zotsatira zomwe timu yake yapeza pomwe yafanana mphamvu 1-1 ndi timu ya Kamuzu Barracks pa bwalo la Chitowe loweruka.
Gondwe anati timu yake inayesesa mpaka kupeza chigoli nthawi yothaitha ndipo akukhulupilira kuti akhale akuchita bwino mu masewero apatsogolo pawo.
"Anali masewero ovuta tithokoze Mulungu kuti tapeza point imodzi. Anzathuwa anachinya patali kwambiri ndipo zimaoneka ngati zitivuta koma sitinatope, tinayesetsa mpaka tinapeza chigoli kutatsala mphindi zitatu." Anatero Gondwe.
Timu ya MAFCO tsopano ili pa nambala 11 ndi point imodzi yomwe ayipeza atasewera masewero awiri mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores