CIVO YAKONZEKA KUKUMANA NDI DEDZA
Timu ya Civo United yati yakonzeka kukumana ndi Dedza Dynamos loweruka likudzali ndipo ikufunitsitsa itapeza chipambano kuti mitima ikhazikike kutimuyi.
Mphunzitsi watimuyi, Abbas Makawa, wati timu yake yamaliza zokonzekera zawo ndipo wati osewera Ake akudziwa kufunikira kopambana pakhomo ndikuti ayiwale kugonja Kwa sabata yatha ndi Mzuzu City Hammers.
"Tamaliza bwino zokonzekera ndipo zayenda bwino kwatsala ndi pabwalo, takonzekera kuti tikachite bwino chifukwa tinagonja mophweka sabata yatha pomwe tinamenya bwino koma sitinapeze chigoli nde mawa tigwira ntchito." Anatero Makawa.
Timu ya Civo inayamba moipa pomwe inagonja 1-0 ndi Mzuzu City Hammers yomwe inangokwanitsa kumenyera pagolo kamodzi kokha basi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores