"ZIGOLI ZAVUMBA KWAMBIRI PA ZOKONZEKERA" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wati timu yake sipita mophweka ku Lilongwe kukakumana ndi Silver Strikers kamba koti mitima ikuwawa ndi kugonja kwa FOMO sabata yatha.
Mphunzitsiyu amayankhula lachisanu pomwe amamalizitsa zokonzekera za masewerowa omwe aliko loweruka pa bwalo la Silver ndipo wati kubwera kwa Clever Chikwata kwapangitsa zokonzekera zawo kukhalanso zabwino.
"Zokonzekera zayenda bwino kwambiri anyamata onse alibwino ndipo akuchilimika ndasiyanitsa ndi za sabata yatha poti panopa zigoli zikuvumba ndipo anyamata ndi owawidwa ndi kugonja ndi FOMO nde masewero awa tikupita kukapambana zikavuta kufanana mphamvu." Anatero Nyambose.
Iye anati Silver Strikers ndi timu yabwino yomwe ili ndi aphunzitsi komanso osewera odziwa ndipo akuipatsa ulemu koma kumbali yawo akonzeka.
Atakumana chaka chatha, Silver inapambana 4-1 ku Lilongwe ndipo Bangwe inapambana 3-2 ku Blantyre.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores