CIVO YATENGA ATATU KU GREEN RANGERS
Timu ya Civo United yamalizitsa zotenga osewera atatu atimu ya Green Rangers, Yankho Biliati, Smey Chimunkho komanso Oscar Luwale omwe amayesa mwayi kutimuyi.
Timu ya Green Rangers yatsimikiza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lake la Facebook ndipo yati osewerawa akhala akuyesa mwayi kwa miyezi iwiri ndipo Abbas Makawa wakhutira ndi ntchito za akatswiriwa.
Pa osewerawa, Billiat ndi Chimunkho amasewera kumbuyo pomwe Oscar Luwale walowa mmalo mwa Lloyd Aaron yemwe wapita ku FCB Nyasa Big Bullets.
Zonse zikatha, timu ya Civo ikhale ikutsimikiza kuti osewerawa asayina migwirizano wa miyezi yochuluka motani.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores