Timu ya Ekhaya United yalowera m'chigawo chapakati masana a tsiku la lero kukachita zokomzekera zamasewero a chaka chino pomwe yakonza masewero opimana mphamvu atatu ndi matimu omwe amasewera muligi ya TNM.
Malingana ndi timuyi yati Lachitatu isewera ndi Silver Strikers pabwalo la Silver kenako Lachinayi ndi Creck Sporting Club ndipo idzatsiliza masewero opimana mphamvuwa Loweluka ndi timu ya Civo Service United.
Mphunzitsi wamkulu watimuyi Jimmy zakazaka wati achita chiganizochi ngati njira imodzi yofuna kukomza timu yamphamvu yomwe isewera ligi ya ThumbsUp Premier Division.
Iye wati akukhulupilira kuti ulendowu uwathandiza kuonaso osewera atsopano omwe timuyi yapeza .
Ekhaya United ,isewera ligi ya ThumbsUp Premier Division Chaka Chino kutsatira kuchita bwino muligi ya Division One Season yatha.
Wolemba: Frank Mojah Dzuwa
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores