EKWENDENI IKUSINTHA DZINA
Timu yomwe imasewera mu ligi ya TNM, Ekwendeni Hammers yalembera kalata bungwe la Football Association of Malawi kupempha kuti isinthe dzina lake.
Timuyi yapanga chiganizo kuti tsopano izitchedwa Mzuzu City Hammers kamba koti omwe amathandiza timuyi amakhala mu mzinda wa Mzuzu chiyambireni kuyithandiza timuyi.
Mlembi watimuyi, Benjamin Thole ndiyemwe watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati padakali pano adikira chilolezo kuchokera ku FAM kuti dzinali lisinthe. Timuyi inalowa mu Supa ligi mu 2019 ndipo ikhala yachiwiri kusintha dzina chaka chino pomwe Kawinga FC inakhala Creck Sporting Club.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores