"OSEWERA AKU MALAWI PHUNZIRANI KWA JORGINHO" - KAYIRA
Wosewera wakale mutimu ya Flames, Chimango Kayira, walandira osewera amdziko muno kuti aphunzirepo pa katswiri watimu ya Arsenal, Jorginho, yemwe tsopano walandira tsamba la uphunzitsi la UEFA B angakhale kuti akusewerabe mpira.
Iye walemba pa tsamba lake la mchezo kuti osewera omwe amafunanso kudzakhala aphunzitsi akhonza kumachitiratu maphunziro ndikuti akadzapuma asadzavutike.
"Anzanga omwe mukusewerabe mpira komanso muli ndi masomphenya odzakhala aphunzitsi, nzotheka kupangiratu mapepala. Generation yathu tinkanyalanyaza ndipo pano tikuwona kuchedwa kuti tifike kumeneku. Anatero Kayira.
Iye anati nzofunikira kukhala ndi aphunzitsi achisodzera omwe ali mu zaka za makumi atatu kapena anayi ndipo kuti zitheke akhonza kumachitiratu panopa.
Jorginho ali ndi zaka 32 ndipo ali mu chaka chake chachiwiri kutimu ya Arsenal pomwe anachokera Ku Chelsea komwe anachitanso zakupsa kumeneko.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores