KAWINGA YALOWA MU LIGI
Zatsimikizika kuti timu ya Kawinga FC isewera mu supa ligi ya 2024 pomwe timu ya Namitete Zitha yakanika kukasuma pa chigamulo chomwe bungwe la Central Region Football Association Inapereka.
Bungwe la Football Association of Malawi lati siliyankhulapo kanthu kamba koti palibe kudandaula kulikonse komwe kwapititsidwa kwa iwo.
Kawinga inamaliza poyamba mu ligi ya Chipiku ndi ma pointsi 53 ndipo chiganizo choti yalowa mu ligi chinayima kaye kamba ka zachinyengo zomwe zinachitika mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores