"TIYESETSA KUTI KACHIKHO KAPENA MWINA LIGI TITENGE" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watsopano kutimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wati ayesetsa kuchita bwino kuti akwanilitse masomphenya atimuyi ofuna kutengako chikho chinachake angakhale ligi ya TNM mu chaka chino.
Iye wayankhula atasaina mgwirizano wa miyezi isanu ndi iwiri nditimuyi lolemba ndipo wati wapita kutimu yomwe imachita kale bwino yomwe akufunitsitsa kuti ichite bwino kuposa pamenepo.
"Zakhala bwino kuti ndapita kutimu yokhazikika kale kusiyana ndi timu yoti ikulowa kumene mu ligi nde nditimu yabwino ya anyamata abwino achisodzera, inathera pa 6, masomphenya atimuyi ndi oti ipite patsogolo nde tilimbikira kuti mwina kachikho titha kutengako mwinakonso ligi imene." Anatero Nyambose.
Mphunzitsiyu wangochotsedwa kumene kutimu ya Mighty Wakawaka Tigers yomwe anathera nayo pa nambala yachikhumi ndi chimodzi (11) mu ligi ya chaka chatha.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores