NYAMBOSE APHUNZITSA BANGWE
Timu ya Bangwe All Stars yalengeza kuti yalemba ntchito mphunzitsi yemwe wangochotsedwa ntchito ku Mighty Tigers, Christopher Nyambose kuti atsogolerere timuyi mu chaka cha 2024.
Timuyi yalengeza mphunzitsiyu lolemba pomwe amasaina mgwirizano wa miyezi isanu ndi iwiri (7) momwenso muli pangano loti athere mkatikati mwa matimu asanu ndi atatu oyambilira mu ligi ya TNM chigawo choyamba chikamatha.
Iye walowa mmalo mwa Abel Mkandawire yemwe mgwirizano wake wa miyezi isanu unatha mu mwezi wa December pamodzi ndi Joseph Kamwendo ndipo timuyi inathera Pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6).
Aphunzitsi onse atimuyi awoneka motere mu 2024:
TECHNICAL DIRECTOR
•Gwaza Chiniko
HEAD COACH
•Christopher Nyambose
ASSISTANT COACH
•Joseph Semu
GOALKEEPERS TRAINER
•Maneno Masowo
TEAM MANAGER
•Steve Madeira
DOCTOR
•Blessings Lapken
SECURITY OFFICER
•Lameck Idana
MEDIA OFFICER
•Richard Tiyesi