BAKA YATENGA KAUNDA NGATI MPHUNZITSI
Mphunzitsi wakale watimu ya Civo United komanso Mighty Mukuru Wanderers, Oscar Kaunda, wasankhidwa kukhala mphunzitsi watimu ya Baka City mu chaka cha 2024.
Timuyi yalengeza za kubwera kwa Kaunda lolemba pomwe akuyamba zokonzekera za ulendo wawo mu ligi ya chaka chino.
Kaunda athandizidwa ndi Davie Muyombe ngati wachiwiri wake yemwe ndi amene analowetsa timuyi mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores