CRFA YAMVERA FAM
Bungwe la Central Region Football Association lamvera mawu a bungwe la Football Association of Malawi pomwe layika masewero otsiriza a pakati pa Kawinga FC komanso Namitete Zitha lamulungu pa bwalo la Nankhaka monga FAM inanenera.
Bungweli limavutavuta kuchititsa masewerowa poti limafuna kuti milandu yomwe ili mu ligiyi yokhudza zachinyengo za masewerowa koma tsopano yamvera FAM.
Mlembi wa CRFA, Antonio Manda, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati wopambana masewerowa sakhala olowa mu TNM Supa ligi poti milanduyi sinathe.
"Nokha munaona FAM inatulutsa kalata kuti masewero aseweredwe koma mtsogoleri wathu anayesetsa kuti asaseweredwe koma zakanika nde sitikufuna kukangana ndi FAM, ndi kholo lathu nde masewero alipo 14:30hrs pa bwalo la Nankhaka. Monga kalata inakambira, opambana sakhala kuti ndi katswiri koma poti masewero anatsala ndi awawa, tikungofuna timalizitse basi kenako tiziunikira milanduyi." Watero Manda.
Padakali pano, Kawinga ili ndi mapointsi 50 ndipo Zit
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores