NKHONDO YA FAM NDI CRFA YAFIKA PA NNONG'A
Bungwe la Football Association of Malawi lati silinamvepo kalata yomwe wapampando wabungwe la Central Region Football Association analemba ponena kuti sinasainidwe ndipo ayitenga ngati yosafunikira.
CRFA inalembera FAM dzulo kuti masewero omwe ali pakati pa Kawinga FC ndi Namitete Zitha samenyedwa kamba koti sanapemphe FAM kuti Ilowelerepo pa nkhaniyi koma FAM yati yabwenza kalatayi.
Iwo ati chomwe ikudziwa ndi choti masewerowa alipo lowerukali ndipo kuti CRFA ilembenso kalata ina yosainidwa bwino kupita Ku FAM isanakwane nthawi ya 12:00hrs masana a lachinayi.
Masewero Ku chigawo chapakati anayima kaye pomwe Namitete Zitha inakamang'ala pa zachinyengo zimene Ngolowindo sinapite ku bwalo la zamasewero zomwe akuti anatumidwa ndi Kawinga FC.
Kawinga ikutsogolera ligiyi ndi mapointsi okwana 50 ndipo Zitha ili pachiwiri ndi 47 pointsi ndipo onsewa atsala ndi masewero amodzi omwe adzakumane.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores