"UYUYU TIMUSWERA PA KAMUZU POMPO" - FOMO
Timu ya FOMO FC yalavula moto ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets Reserve ponena kuti ibwere mokonzeka chifukwa ayigonjetsanso pomwe akukumana lero mmasewero achibwerenza a ndime yamatimu anayi a Ligi ya Southern Region pa bwalo la Kamuzu lero.
Mphunzitsi watimuyi, Fadweck Sosten, wati masewerowa akhala ophweka kwambiri poti akudziwa mmene atayigonjetsere angakhale kuti zipambano pa bwaloli zimavuta.
“Abwana likamatha tsiku la lero Bullets Reserve tiyibatiza ndi zigoli zodutsa ziwiri. Tilibe mantha aliwonse anyamata akonzeka kugwira ntchito yomwe tawatuma.Pa Kamuzu ndi panyumba pathu ndiwapemphe anthu abwere mwamkokomo tidzawapatsa mpira wabwino.” Sosten amayankhulana ndi Frank Mojah Dzuwa.
FOMO ipita mmasewerowa ikutsogola 2-0 yomwe anapambana lamulungu lapitali pa bwalo la Esparanza ku Mulanje. Yemwe adutse lero akumana ndi Ntopwa mu ndime yotsiriza pa 28 January 2024.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores