"CHAKHALA CHAKA CHABWINO KWA INEYO" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, Macdonald Mtetemera, wati chaka cha 2023 chakhala chopambana kwambiri kwa iyeyo ndi timuyi pomwe wati wakwanitsa kufika malo omwe samayembekezera.
Iye amayankhula izi atatha masewero omwe agonja 4-3 pa mapenate ndi Bangwe All Stars kuti atuluke mu chikho cha Castel ndipo Mtetemera wati ndi zowawa koma sizinayipe kwenikweni.
"Kwa ineyo chakhala chaka chabwino kwambiri mwina mu chikho Ichichi timafuna titafika patali koma tathera pa ndime ya matimu asanu ndi atatu komanso mu ligi tathera pachinayi nde yakhala yabwino tikangokonza mwina ndi mwina kuti chaka cha mawa tidzabwere mwa mphamvu." Anatero Mtetemera.
Chitipa inali imodzi mwa matimu omwe alowa mu ligiyi mmene timayamba chakachi koma yagonjetsako matimu akuluakulu ngati Wanderers komanso Bullets.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores