"WANDERERS IKUVUTIKA CHIFUKWA CHA NKHAKANANGA" - AKATSWIRI
Akatswiri pa nkhani zamasewero mdziko muno awopseza kuti nkhani ya Mighty Mukuru Wanderers komanso Football Association of Malawi yokhudza chigamulo pa masewero amu chikho cha Airtel Top 8 kukhonza kuipitsa mayina a omwe amathandiza timuyi.
Izi ayankhula ndi Ojuku Malunga komanso Peter Fote pa Times 360 Sports lolemba ndipo ati timu ya Wanderers ikuvutika pomwe anaononga ndi Godfrey Nkhakananga.
"Nkhakananga chilango chake chatsala pang'ono pomwe Wanderers ikadalibe kuvutika, mwina tsopano tivomereze kuti oyimbira pa dziko lonse la pansi sali bwino, tinaziona mmasewero ambiri mu Premier league komabe iwowa lamulo likumawateteza." Anatero Fote.
Awiriwa ati akanakondabe kuti nkhaniyi Nkhakananga awunikidwebe koma akanakonda kuti nkhani tsopano ithe kuti mpira wa mdziko muno uyende bwino. Padakali pano, Wanderers yakamang'alanso pa chiganizo cha FAM poyilangabe timuyi.
Source: Times
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores