MASEWERO A WANDERERS NDI SILVER AKADALI PA 25 NOVEMBER
Bungwe la Football Association of Malawi latulutsa masiku omwe masewero awiri amu chikho cha Airtel Top 8 aseweredwe komanso mabwalo ake.
Bungweli latsimikiza kuti timu ya Mighty Mukuru Wanderers ikumanabe ndi Silver Strikers loweruka likudzali pa bwalo la Kamuzu mu masewero achibwereza a mu ndime ya matimu asanu ndi atatu ngakhale kuti Wanderers yakasumabe posagwirizana ndi chiganizo cha bungweli.
Wanderers ikutsutsana ndi chiganizo choti inagonja 2-0 kamba koti inatuluka mu bwalo la zamasewero asanathe komanso kuti apereke K24.5 million kamba kophwanya mipando ya pa bwalo la Bingu.
Ndipo masewero oyamba a ndime ya matimu anayi iliko lamulungu pakati pamatimu a Blue Eagles ndi FCB Nyasa Big Bullets omwe akumane pa bwalo la Bingu lamulungu likudzali.
Opambana pakati pa Wanderers ndi Silver adzakumana ndi MAFCO komatu tsiku ndi bwalo zilengezedwabe kutsogoloku.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores