"SITIKUYANG'ANA ZOTSALA MU LIGI KOMA TOP 8" - MAULUKA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Ekwendeni Hammers, Luckson Mauluka Nyoni, wati chipambano chomwe timuyi yapeza chiwathandiza kubweretsanso mtima wopambana kwa osewera pomwe akuyang'ana zoyambiranso kuchita bwino mu ligi ya TNM.
Mauluka amayankhula izi pomwe timuyi yapambana koyamba mu chigawo chachiwiri pomwe yagonjetsa Extreme FC pa bwalo la Rumphi. Iye wati ndi okondwa kamba ka chipambanochi ndipo zibwenzeretsa mtima wopambana kwa osewera atimuyi.
"Ndife okondwa kamba ka chipambanochi chimene takhala tikuchifuna kwambiri, kupambana kwa lero kutithandiza kuti anyamata abweremo mzimu opambana poti pakatipa anasiya kuzikhulupilira. Sitikuyang'ana zotsala mu ligi komatu kutsala mu top 8." Anatero Mauluka.
Pa masewero 21 yomwe asewera atimuyi, Ekwendeni Hammers yapeza mapointsi okwana 28 ndipo ili pa nambala yachisanu ndi chitatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores