"MWANA WOPANDA KHALIDWE PAKHOMO, KUNJA SATENGEDWA" - MATAYA
Mmodzi mwa anthu otsatira nkhani zamasewero mdziko muno, Mussa Mataya, wati ndi zovuta kuti oyimbira amdziko muno azitengedwa pa mipikisano yaikuluikulu pa dziko lonse poti amadandaulidwa angakhale ndi kwawo komwe.
Mataya wayankhula izi kutsatirakusapezeka kwa oyimbira aku Malawi pa ndandanda wa oyimbira omwe asankhidwa ndi bungwe la CAF kuti akaphunzitse maphunziro apadera patsogolo pa mpikisano wa AFCON. Iye wati kuli zambiri zomwe oyimbira akufunika akonze.
"Ndikukhulupilira kuti sizachilendo chifukwa chiyambireni ligi ya chaka chino, matimu akungodandaulabe kamba kosaimbira bwino nde zimene zija zimapita patali ndipo zikutsekereza mi mwayi yawo kunjaku." Anatero Mataya ndi Owinna.
Oyimbira 75 ndi omwe akutenga nawo mbali pa maphunzirowa ndipo palibepo aliyense waku Malawi yemwe watengedwapo.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores