BUNGWE LA NRFA LAPEREKA CHILANGO KWA BWABWA FC
Timu ya mu ligi yaying'ono ya kumpoto ya Bwabwa FC yapatsidwa chilango chosasewera masewero aliwonse a bungwe la Northern Region Football Association atapezeka olakwa pa mlandu omenya oyimbira.
Mu kalata imene bungweli latulutsa lachiwiri, komiti ya bungweli yapeza kuti timuyi inamenya oyimbira pa masewero amu chikho cha Castel Challenge pomwe anakumana ndi Ekwendeni United pa bwalo la Ekwendeni ndipo ochemerera anamenya oyimbira ati amakondera.
Oyimbirawa anapititsidwa ku chipatala komwe anakathandizidwa ndipo bungweli lati mchitidwewu ukhonza kuchotsa moyo wa munthu ndipo wapereka chilangochi kuti aphunzirepo.
Iyi ndi timu yachiwiri kulandira chilango ngati ichi ndi bungweli pomwe Chintheche United inalandira chilango chosasewera kwa zaka ziwiri pa milandu ngati yomweyi. Bwabwa ili ndi maola 48 ngati ikufuna kukasuma posagwirizana ndi chigamulochi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores