TIFINYE MAKOLONA POMWE KAMUZU ILI PA NGOZI
Bwalo la Kamuzu ili pa ngozi yoti itha kutsekedwa pomwe bungwe la Football Association of Malawi likuyendera bwaloli kuti lipeze ngati lili lotetezeka kuchititsa masewero a mpira.
Izi zili chomwechi kamba koti bungweli latseka mabwalo awiri a Civo ndi Mzuzu sabata yatha kamba koti sali bwino ndipo akufunika kukonzedwa.
Sabata ino, FAM ikuyendera mabwalo ena mdzikomu ndipo lachiwiri, ayendera bwalo la Kamuzu lomwe mwazina lili kale pangozi chifukwa linaletsedwa kuchititsa masewero ndi matimu akunja ndi bungwe la CAF ndipo FAM inaletsa bwaloli kuchititsa masewero a matimu akuluakulu ngakhale kuti SULOM linanyozera ndikuchititsa masewero a Bullets ndi Wanderers.
Pakadali pano, zotsatira za kuyenderaku zidziwika masabata awiri akudzawa ndipo litha kutsekedwa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores