MOYALE IKUPITA KU ZIMBABWE
Timu ya Moyale Barracks ikunyamuka mmawa wa lero pa bwalo la ndege la Kamuzu International kulowera mdziko la Zimbabwe komwe akasewerako masewero apaubale ndi timu yachisilikali kumeneko.
Timuyi yaitanidwa ndi asilikali aku Zimbabwe omwe akusangalalira kuti atha zaka 30 ndipo anapempha asilikali aku Malawi kuti atumize timu yachisilikali imodzi kuti akawathandize kusangalala.
Mphunzitsi watimuyi, Nicolas Mhango, wati ulendowu ndi wofunikira kutimu yawo pomwe akatengako upangiri wapaderadera mu dzikoli zimene ziwathandize mu ligi ya Chaka chino.
Mu ligi ya chaka chino, Moyale ili pa nambala yachisanu ndi chinayi (9) pomwe inatolera mapointsi 19 pamasewero 16 omwe yasewera. Timu ya Kamuzu Barracks ndi yokhayo yachisilikali yomwe ili pamwamba pawo pomwe ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6).
Source: Moyale Website
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores