"BULLETS IKUPANGA ZA BULLETS" - MUNTHALI
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali, wati timu yake sikuyang'ana kuti ili pambuyo pa matimu ena mu ligi ya TNM pomwe akungosewera masewero ngati Bullets basi.
Munthali amayankhula izi patsogolo pa masewero awo ndi timu ya MAFCO ku Chitowe pomwe wati timu yawo yakonzekera kwambiri mmasewerowa.
"Masewero alipodi pafupifupi komabe ndi masewero osiyana, anyamata timawauzanso zisiyana, ya ligi timawauza zina ya cup zina komanso kuyenda kwachuluka nde anyamata akumatopa mchifukwa chake tikudalira anyamata onse." Anatero Munthali.
Iye wati MAFCO ndi timu Ina yomwe amavutitsana nayo koma awonetsetsa kuti pakutha pa masewero, iwo atenge chipambano. Iye wati Alick Lungu ndi Stanley Biliati sapezeka kamba kuvulala koma wati Ernest Petro akumuunikabe.
Bullets ikapambana ifika pa nambala yoyamba mu ligiyi pomwe ikhale ndi mapointsi 33 pa masewero 16.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores