KAMWENDO WAKONDWA NDI CHIPAMBANO CHOYAMBA
Mphunzitsi wogwirizira watimuyi ya Bangwe All Stars, Joseph Kamwendo, wati ndi okondwa kamba kopeza chipambano mmasewero omwe timuyi yagonjetsa Mighty Wakawaka Tigers 0-1 pa bwalo la Mpira pomwe wati ndi chiyambi cha zabwino.
Kamwendo wati timu yake inasewera mwapamwamba koma wadandaula ndi kutaya mipata yambiri zomwe akuti zikufunika kukonza.
"Ndi chipambano chokoma kwambiri, anyamata asewera bwino koma taluza mipata yochuluka yomwe imafunikira kudekha koma amafulumira kapena kuchedwa nde tibwerera tikakonze." Anatero Kamwendo.
Iye watinso timu yake iyendayenda kuti ipeze anyamata ena oti awonjezere mphamvu. Bangwe tsopano yafika pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe Tigers yaimabe pa nambala 14.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores