MADINGA WASAINA KU WANDERERS
Timu ya Mighty Mukuru Wanderers yalengeza za kubwereranso kwa Francisco Madinga kutimuyi pomwe katswiriyu wasaina mgwirizano wa zaka ziwiri ndi timuyi lachiwiri.
Madinga wabwerera kutimuyi kutsatira kukhala opanda timu atathetsa mgwirizano wake ndi timu yaku Jwaneng Galaxy yaku Botswana mmiyezi iwiri yapitayo.
Madinga wakhala akupanga zokonzekera ndi timuyi kuchokera sabata yatha ndipo akhonza kuoneka mmasewero atimuyi ndi Red Lions lachitatu mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores