"NDIKADAPHUNZIRABE" - KONDOWE
Katswiri wa timu ya FCB Nyasa Big Bullets wati akufunitsitsa atachita zambiri kutimuyi pomwe wati sanafikepo pomwe iye akufuna.
Kondowe amayankhula izi ndi Mtolankhani wathu, Hastings Kasonga, pomwe wati ndi okondwa ndi mmene akuchitira koma akadaphunzirabe kuti akhale pabwino.
"Sindinafikepo penipeni pa ine komano ndikadaphunzirabe kuchokera kwa mphunzitsi wabwino kwambiri nde ndikufunitsitsa kuti ndichitebe bwino ndi Bullets." Iye anatero.
Kondowe wakhala ofunikira kumbali ya timuyi pomwe kwa sabata yathayi wayipulumutsa kawiri konse mmasewero awo ndi Mighty Wakawaka Tigers komanso Extreme FC pomwe anapeza zigoli atachokera panja.
Iye anapita kutimuyi atachotsedwa ku Mighty Mukuru Wanderers komwe anangokhalako chaka chimodzi ndi kusewera masewero atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores