DEDZA YATOLA THANDIZO LA K5 MILLION
Timu ya Dedza Dynamos yatola thumba la ndalama pomwe mwini wake wa Amazing Grace Christian Church, M'busa Chimwemwe Chafumuka walonjeza kupereka thandizo la ndalama zokwana K5 million pa miyezi khumi.
M'busayu walengeza nkhaniyi lolemba pomwe wati akhale akuthandiza timuyi ndi K500,000 pa mwezi uliwonse kwa miyezi khumi ndi cholinga choti timuyi ipitilire kuchita bwino mu ligi ndi zikho.
Gawo la ndalamazi zikhalenso zikugwira ntchito popereka K100, 000 kwa osewera yemwe wachita bwino kuposa anzake mwezi wina uliwonse kutimuyi.
Dedza ili mundime yamatimu anayi mu chikho cha FDH Bank ndipo timuyi ilipanambala yachisanu ndichitatu mu TNM Super league ndimapointi 19 pokutha pa chigawo choyamba.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores