"OYIMBIRA WATIPWETEKA KWAMBIRI." - KANANJI
Mphunzitsi watimuyi ya Blue Eagles, Eliya Kananji, wadandaula ndi kayimbilidwe ka oyimbira mmasewero awo ndi timu ya Silver Strikers kuti awapweteka pomwe wati ziganizo zake zimadana ndi Blue Eagles.
Kananji anayankhula zimenezi atatha masewero omwe Eagles yagonja 2-1 ndi timu ya Silver Strikers pa bwalo la Bingu. Iye akuganiza kuti oyimbira mtsikuli anangochikonza kuti akhaulitse timu yake.
"Chigoli choyamba chinali cha offside koma oyimbira sanapangepo kalikonse ndipo tachinyitsa Chachiwiri, chinali cha bwinobwino ndithu kenako tinabweramo ndipo tinagoletsa chigoli ndipo tapeza penate koma oyimbira kutikanira." Anatero Kananji.
Malingana ndi kanema yemwe akuyenda pa tsamba la mchezo, Chinsisi Maonga wa Silver Strikers anagwira mpira mu box koma oyimbira anapereka kuti ndi omwenya ndi mwendo panja pa bokosi.
Chinsisi Maonga ndi Stain Davie ndi omwe anagoletsa zigoli za Silver Strikers kuti ifike pamwamba pa ligi ndi mapointsi 32.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores