"MWINA MMIYEZI ITATUYI ANTHU ADZAKAMBA ZA IFE" - NGINDE
Mphunzitsi watimu ya Chitipa United, MacDonald Mtetemera, wapempha akuluakulu a timuyi komanso ochemerera ake kuti akhale ogwirizana kuti mwina akhonza kudzatenga chikho cha TNM Supa ligi mu December.
Mtetemera anayankhula izi atatha masewero awo omwe anagonjetsa Karonga United 2-0 ndi zigoli za Ramadan Mtafu komanso China Chirwa. Iye anati timu yake yonse ilindi anyamata odziwa omwe akugwira ntchito yapamwamba.
"Anyamatawa akumvera chimene tikuwauza ndipo tili ndi anyamata abwino, masewero aliwonse tikumasintha atatu anayi koma akuchitabe chimodzi, tingopempha mgwirizano kutimuyi kuti mwina mwina mmiyezi ikudzayi anthu nkudzakamba za Chitipa." Anatero Nginde.
Timu ya Chitipa ili pa nambala yachiwiri mu ligi pomwe yatolera mapointsi 32 pa masewero 16 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores