"WANDERERS ILI NGATI MIKANGO YA NJALA YA MIYEZI ITATU" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati akuyembekezera kuti akakumana ndi masewero ovuta pomwe akukonzekera kukumana ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers komabe wati akonza mavuto awo.
Iye wayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aliko loweruka likudzali pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akonza kuti adzateteze pagolo pawo komanso kukwanitsa kupeza zigoli.
"Tikuyembekeza masewero ovuta poti Wanderers ili ngati mikango yomwe siyinadye kwa miyezi itatu nde ndi mmene tikukonzekerera kuti tikufuna tikapite kutsogolo kwambiri komanso kumbuyo kwathu tisakachinyitse nde anyamata alibwino." Iye watero.
Iye watinso katswiri wawo, Promise Kamwendo sapezeka kamba koti ndi wovulala ndipo asowa kwa masamba atatu.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ali ndi mapointsi Khumi ndi imodzi (11) pa masewero 8
ZOONA
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores