"TAKONZA MAKA KUTSOGOLO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO, Gilbert Chirwa, wati timu yake yaunikira mavuto awo onse omwe anavutika mmasewero omwe anagonja ndi Creck Sporting Club sabata yatha ndipo akuyembekezera kuchita bwino loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi MAFCO pa bwalo la Chitowe ndipo wati iwo akonzeka.
"Takonzekera bwino kwambiri masewerowa ndipo molalo ili pamwamba pakati pa anyamatawa. Tawunikira monse momwe timafooka maka kutsogolo ndipo ndikukhulupilira tikachita bwino." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO ili pa nambala 12 pomwe ili ndi mapointsi 7 pa masewero 7 omwe yasewera mu ligiyi.
koma munditumiziladi?
@emanuel.mateus takutumizirani. Pepani tachedwetsa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores