"BULLETS SINAPEZEKO MPATA WENIWENI" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC Enos Chatama wati sanadandaule ndi zotsatira za masewero awo ndipo wayamikira osewera ake kamba kosewera mwapamwamba angakhale kuti aphonya mipata ingapo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 0-0 ndi FCB Nyasa Big Bullets ndipo wati anali masewero omwe mitima inali mmwamba komanso ziganizo zina zolakwika.
Iye wati timu yake inayesetsa kusewera mwapamwamba kuti apeze zigoli koma zinavuta komabe sakudandaula ndi zotsatirazi.
"Ndi anyamata chabe oti akuphunzira, lero taonapo malo atatu oti tikakonze ndiye tikhalabe tikumanga timu kuti 2027 tidzakhale ndi timu yokhazikika ndipo 2028 tizidzalimbirana zikho," anatero Chatama.
Kutsatira kupeza point imodzi, timuyi yafika pa nambala yachisanu pomwe ili ndi mapoints 16 pa zipambano zinayi, kufanana mphamvu kanayi ndi kugonja kawiri.
0991769328
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores