Bungwe loyendetsa ligi ya TNM la Super League of Malawi (Sulom) lakana pempho la timu ya Ntopwa kuti matimu omwe sanachite bwino chaka chino asatuluke mu ligiyi.
Mtsogoleri wa bungweli, Tiya Somba Banda ndiye wanena izi.
Malingana ndi a Banda zomwe timu ya Ntopwa imapempha ndi zosephana ndi malamulo oyendesera ligi ya TNM.
Izi zikutanthauza kuti matimu a Mzuzu Warriors, Ntopwa ndi timu ina yomwe ithere pa number 14 atuluka mu ligiyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores