KARONGA YADANDAULA NDI OYIMBIRA KOMANSO MASAPOTA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United Chrispin Chimkwita wadandaula ndi kayimbilidwe ka oyimbira pa masewero awo ndi Silver Strikers komanso masapota a Silver omwe akuti anawaopsera ndi kulimbana nawo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 4-1 pa bwalo la Silver ndipo iye anayankhula mwa chining'a kuti oyimbira akamayimbira monga anachitira ndekuti masewero apita patsogolo mdziko muno.
"Mchigawo chachiwiri tinayamba mosiyana ndi choyamba zomwe zinatipangitsa kugona komabe tiyamikire oyimbira kuti ayimbira bwino, atamatero mpira utha kupita patsogolo komanso ochemerera kulimbana nafe tingoti tisayankhule kwambiri," iye anatero.
Pambali pa zonsezi, Chimkwita anatibe ndi okondwa ndi mmene timu yake ilili kunena kuti ali ndi timu yabwino.
Timuyi tsopano yatsika kufika pa nambala 13 ndi mapoints asanu ndi anayi pamaseweronso asanu ndi anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores