"NDILI NDI CHIKHULUPILIRO KUTI TIKAGOLETSA" - ZOYA
Wachiwiri kwa mphunzitsi watimu ya Civil Service United Emmanuel Zoya wati timu yake inayika chidwi chachikulu pa kugoletsa komanso kuchinjiliza mkati mwa sabatayi ndipo ali ndi chikhulupiliro kuti akagoletsa zambiri kuti apambane loweruka.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Mighty Wanderers pa bwalo la Civo ndipo wati akuyembekezera kupeza chipambano pa masewerowa.
Iye anati timu yawo yakhala isakuchita bwino mu masewero awo angapo mu ligi koma akhala pansi ndi kuunikirana kufunika koti ayambe kuchita bwino.
"Takhala tikumachinyitsa kwambiri komanso kukanika kuchinya nde ndi zomwe anyamata akonzekeretsedwa patsogolo pa masewero moti tikachita bwino," anatero Zoya.
Iye anatinso timu yake yakhudzidwa ndi kuvulala kwa osewera chaka chino koma pamenepo sipakhala pothawira poti ali ndi osewera ochuluka.
Timuyi ili pa nambala 10 mu ligi pomwe ili ndi mapoints 11 pa masewero 9 omwe asewera mu ligi.
📷 Civil media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores