"MU MPIRA KULIBE KUBWENZERA" - CHATAMA
Mphunzitsi watimu ya Ekhaya FC Enos Chatama wati mu masewero ampira wamiyendo kulibe zoti timu ina imabwenzera chipongwe inzake koma kuti yomwe yakonzekera bwino ndi imene imapambana pa masewero.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero atimuyi ndi FCB Nyasa Big Bullets lamulungu pa bwalo la Mpira ndipo anakumananso Sabata yatha mu masewero a chikho omwe Ekhaya inapambana.
Iye wati akuyembekezera masewero ovuta kwambiri poti Bullets idzabwera mwa mphamvu koma timu yake ndi yokonzeka pa masewero amenewa.
"Palibe phuma lomwe tiwapatse osewera athu patsogolo pa masewero amenewa chifukwa tili ndi masewero ochuluka kwambiri komanso Ife sitikuyang'ana ligi koma kuwalimbikitsa osewera athu kuti azisewera bwino," anatero Chatama.
Iye wamenanso ochemerera a timuyi kufika mwa unyinji kuti adzawapatse mphamvu pa masewerowa.
Ekhaya ilowa mu masewerowa ili pa nambala yachisanu pomwe ili ndi mapoints 15 pa zipambano zinayi, kufananitsa mphamvu katatu ndi kug
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores