MPINGANJIRA SADZAYIMA KU FAM
Mtsogoleri wa timu ya Ekhaya FC William Mpinganjira sadzayimira pa mpando wa utsogoleri wa bungwe la Football Association of Malawi mu chaka cha 2027 pa zisankho za bungweli.
Izi zadziwika kutsatira chibaluwa chomwe timuyi yatulutsa lachisanu chosainidwa ndi mkulu wa ogwira ntchito kutimuyi Thando Mhango chofotokoza kuti mphekesera zimene zakhala zikumveka ndi zabodza.
Iye wati anthu ena adzalemba pa 20 June 2026 kuti Mpinganjira ayima nawo kuti adzapikisane ndi a Fleetwood Haiya pa mpandowu koma iwo ati mkuluyu waika chidwi chofuna kukweza timu ya Ekhaya Kuti ikhale yaikulu kwambiri m'dziko muno.
Iye wapemphanso masapota a timuyi kukhala kutali ndi mphekeserazi poti onse ndi okhumbira kuti ntchito za timuyi zipite patsogolo.
Mmbuyomu a Mpinganjira adanenanso kuti sakufuna kudzapikisana nawo pa mpandowu ndipo uku ndi kubwerenza kwa uthengawu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores